Ngati wina kundendeko amakonzekera kuti tsiku lina adzakhala mesho wa a Saulos Chilima asiyiletu. Milandu yawo yonse ija a boma aithetsa. Tsopano ndi mfulu. Bwalo la milandu lero pa 6 May lavomereza pempho lochoka kwa mkulu oyimba milandu oti milandu ya katangale yokhudza wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ithe.