Mtsogoleri wa bungwe la National Women’s Football a Adelaide Migogo wati mphoto imodzi yomwe Malawi yapeza yomwe wawina Leticia Chinyamula kukhala osewela yemwe adzakhale wapamwamba mtsogolomu zawonetsa kuti osewerawa ali ndi kuthekera kochita bwino kwambiri mtsogolomu akamalowa nawo mu mipikisano yambiri.